4 Muzicita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
5 Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawacita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.
6 Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wacekumbvula; Ine ndine Yehova.
7 Usamabvula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamambvula.
8 Usamabvula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.
9 Usamabvula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.
10 Usamabvula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako.