2 Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi libano wace wonse; ndipo wansembeyo aitenthe cikumbutso cace pa guwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
3 Ndipo cotsalira ca nsembe yaufa cikhale ca Aroni ndi ana ace; ndico copatulikitsa ca nsembe zamoto za Yehova.
4 Ndipo ukabwera naco copereka ndico nsembe yaufa, yophika mumcembo, cizikhala ca timitanda ta ufa wosalala topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda cotupitsa todzoza ndi mafuta.
5 Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m'ciwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda cotupitsa, wosanganiza ndi mafuta.
6 Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa.
7 Ndipo copereka cako cikakhala nsembe yaufa ya mumphika, cikhale ca ufa wosalala ndi mafuta.
8 Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera naco kwa wansembe, iyeyo apite naco ku guwa la nsembe.