20 Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa atate wace, nabvula mbale wa atate wace; asenze kucimwa kwao; adzafa osaona ana.
21 Munthu akatenga mkazi wa mbale wace, codetsa ici; wabvula mbale wace; adzakhala osaona ana.
22 Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwacita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo.
23 Musamatsata miyambo ya mtundu umene neliucotsa pamaso panu; popeza anacita izi zonse, nelinalema nao.
24 Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu yina ya anthu.
25 Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kali konse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.
26 Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.