1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu cifukwa ca wakufa mwa anthu a mtundu wace;
2 koma cifukwa ca abale ace eni eni ndiwo, mai wace, ndi atate wace, ndi mwana wace wamwamuna, ndi mwana wace wamkazi, ndi mbale wace;
3 ndi cifukwa ca mlongo wace weni weni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse cifukwa ca iwowa.
4 Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wace, asadzidetse, ndi kudziipsa,
5 Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kucecerera ndebvu zao, kapena kudziceka matupi ao.