1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2 Nena ndi Aroni ndi ana ace amuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.
3 Nena nao, Ali yense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azipatulira Yehova, pokhala ali naco comdetsa cace, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.
4 Munthu ali yense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo ali yense wokhudza cinthu codetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;
5 ndi ali yense wokhudza cinthu cokwawa cakudetsedwa naco, kapenanso munthu amene akamdetsa naco, codetsa cace ciri conse;