18 Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, ana a nkhosa asanu ndi awiri, opanda cirema a caka cimodzi, ndi ng'ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.
19 Mukonzenso mwana wa mbuzi mmodzi akhale nsembe yaucimo, ndi ana a nkhosa awiri a caka cimodzi akhale nsembe yoyamika.
20 Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi ana a nkhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.
21 Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.
22 Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.
23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
24 Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko cikumbutso ca kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.