1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2 Uza ana a Israyeli, kuti akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti aziwalitsa nyali nthawi zonse.
3 Aroni aikonze kunja kwa nsaru yocinga ya mboni, m'cihema cokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.
4 Akonze nyalizo pa coikapo nyali coona pamaso pa Yehova nthawi zonse.
5 Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi,
6 Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.