3 Aroni aikonze kunja kwa nsaru yocinga ya mboni, m'cihema cokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.
4 Akonze nyalizo pa coikapo nyali coona pamaso pa Yehova nthawi zonse.
5 Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi,
6 Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.
7 Nuike libano loona ku mzere uli wonse, kuti likhale kumkate ngati cokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.
8 Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, cifukwa ca ana a Israyeli, ndilo pangano losatha.
9 Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ace, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulikitsa wocokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.