4 Akonze nyalizo pa coikapo nyali coona pamaso pa Yehova nthawi zonse.
5 Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi,
6 Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.
7 Nuike libano loona ku mzere uli wonse, kuti likhale kumkate ngati cokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.
8 Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, cifukwa ca ana a Israyeli, ndilo pangano losatha.
9 Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ace, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulikitsa wocokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.
10 Ndipo mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeli, atate wace ndiye M-aigupto, anaturuka mwa ana a Israyeli; ndi mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeliyo analimbana naye munthu M-israyeli kucigono;