1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi kuti,
2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira Yehova Sabata.
3 Zaka zisanu ndi cimodzi ubzale m'munda mwako, ndi zaka zisanu ndi cimodzi udzombole mphesa zako, ndi kuceka zipatso zace;
4 koma caka cacisanu ndi ciwiri cikhale sabata lakupumula la dziko, sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako.
5 Zophuka zokha zofikira masika usamazichera, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usaziceka; cikhale caka copumula dziko.
6 Ndipo sabata la dzikoli likhale kwa inu la cakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa nchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;
7 ndi ng'ombe zako, ndi nyama ziri m'dziko lako; zipatso zace zonse zikhale cakudya cao.