45 Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anu anu.
46 Ndipo muwayese colowa ca ana anu akudza m'mbuyo, akhale ao ao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israyeli, musamalamulirana mozunza.
47 Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera cuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa pfuko la banja la mlendo;
48 atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ace amuombole;
49 kapena mbale wa atate wace, kapena mwana wa mbale wa atate wace amuombole, kapena mbale wace ali yense wa banja lace amuombole; kapena akalemera cuma yekha adziombole yekha.
50 Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira caka adadzigulitsa kwa iye kufikira caka coliza lipenga; ndipo mtengo wace ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.
51 Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndarama zakumuombola zocokera ku ndalama zomgulazo.