24 Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zoipa zanu.
25 Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakucita cilango ca cipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.
26 Pamene ndityola mcirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mcembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.
27 Ndipo mukapanda kundimvera Ine, cingakhale ici, ndi kuyenda motsutsana nane;
28 Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.
29 Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya.
30 Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.