38 Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.
39 Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.
40 Pamenepo adzabvomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pocita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,
41 Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzicepetsa, ndipo abvomereza kulanga kwa mphulupulu zao;
42 pamenepo ndidzakumbukila pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isake, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukila; ndipo ndidzakumbukila dzikoli.
43 Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ace, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzabvomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.
44 Ndiponso pali icinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kutyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Muhmgu wao.