14 Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika.
15 Kunena za nyama ya nsembe volemekeza ya nsembe zoyamika zace, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa.
16 Koma nsembe ya copereka cace ikakhala ya cowinda, kapena copereka caufuhi, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yace; ndipo m'mawa adye cotsalirapo;
17 koma cotsalira pa nyama ya nsembeyo tsiku lacitatu, acitenthe.
18 Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zace tsiku lacitatu, sikubvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo cinthu conyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zace.
19 Ndipo nyama yokhudza kanthu kali konse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama yina, ali yense ayera aidyeko.
20 Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala naco comdetsa, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.