19 Ndipo nyama yokhudza kanthu kali konse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama yina, ali yense ayera aidyeko.
20 Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala naco comdetsa, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.
21 Ndipo munthu akakhudza cinthu codetsa, codetsa ca munthu, kapena codetsa ca zoweta, kapena ciri conse conyansa codetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.
22 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
23 Lankhula ndi ana a Israyeli ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng'ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi.
24 Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi cirombo ayenera nchito iri yonse, koma musamadya awa konse konse.
25 Pakuti ali yense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.