22 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
23 Lankhula ndi ana a Israyeli ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng'ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi.
24 Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi cirombo ayenera nchito iri yonse, koma musamadya awa konse konse.
25 Pakuti ali yense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.
26 Ndipo musamadya mwazi uti wonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse,
27 Ali yense akadya mwazi uti wonse, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.
28 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,