24 Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi cirombo ayenera nchito iri yonse, koma musamadya awa konse konse.
25 Pakuti ali yense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.
26 Ndipo musamadya mwazi uti wonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse,
27 Ali yense akadya mwazi uti wonse, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.
28 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
29 Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yace kwa Yehova, azidza naco copereka cace kwa Yehova cocokera ku nsembe yoyamika yace;
30 adze nazo m'manja mwace nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.