33 nawakantha kuyambira ku Aroeri mpaka ufika ku Miniti, ndiyo midzi makumi awiri, ndi ku Abelikerami, makanthidwe akuru ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israyeli.
34 Pofika Yefita ku Mizipa ku nyumba yace, taonani, mwana wace wamkazi anaturuka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wace mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.
35 Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zobvala zace, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukuru, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.
36 Ndipo anati kwa iye, Atate wanga, mwamtsegulira Yehova pakamwa panu, mundicitire ine monga umo mudaturutsa mau pakamwa panu; popeza Yehova anakucitirani inu cilango pa adani anu, pa ana a Amoni.
37 Ndipo anati kwa atate wace, Andicitire ici, andileke miyezi iwiri, kuti ndicoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga.
38 Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzace, nalirira unamwali wace pamapiri.
39 Ndipo kunali pakutha miyezi iwiri, anabwerera kwa atate wace amene anamcitira monga mwa cowinda cace anaciwinda; ndipo sanamdziwa mwamuna. Motero unali mwambo m'Israyeli,