1 Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israyeli, panali munthu Mlevi wogonera kutseri kwa mapiri a Efraimu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda.
2 Koma mkazi wace wamng'ono anacita cigololo akali naye, namcokera kumka ku nyumba ya atate wace ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.
3 Koma anauka mwamuna wace namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wace, ndi aburu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye ku nyumba ya atate wace. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo, anakondwera kukomana naye.
4 Ndipo mpongozi wace, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.
5 Ndipo kunali, tsiku lacinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kucoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wace, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.
6 Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Ubvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.
7 Ndipo munthuyo ananyamuka kuti amuke; koma mpongozi waceyo anamkakamiza, nagonanso komweko.