6 Ndipo amuna a ku Gibeoni anatumira Yoswa mau kucigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.
7 Pamenepo Yoswa anakwera kucokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi yose.
8 Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.
9 Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kucokera ku Giligala usiku wonse.
10 Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israyeli, ndipo anawakantha makanthidwe akuru ku Gibeoni, nawapitikitsa pa njira yokwera ya Betihoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.
11 Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israyeli, potsikira pa Betihoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikuru yocokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anacuruka ndi iwo amene ana a Israyeli anawapha ndi lupanga.
12 Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israyeli; ndipo anati pamaso pa Israyeli,Dzuwa iwe, linda, pa Gibeoni,Ndi Mwezi iwe, m'cigwa ca Aialo.