6 nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebano, mpaka Misirepotumaimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israyeli, koma limeneli uwagawire Aisrayeli, likhale colowa cao, monga ndinakulamulira.
7 Ndipo tsopano uwagawire mapfuko asanu ndi anai, ndi pfuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale colowa cao.
8 Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira colowa cao, cimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordano kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;
9 kuyambira pa Aroeri, wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uti pakati pa cigwa, ndi cidikha conse ca Medeba mpaka ku Diboni;
10 ndi midzi yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, wakucita ufumu m'Hesiboni, mpaka malire a ana a Amoni;
11 ndi Gileadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Herimoni, ndi Basana ionse mpaka ku Saleka;
12 ufumu wonse wa Ogi m'Basana, wakucita ufumu m'Asitarotu, ndi m'Edrei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefai); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.