16 Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha Kiriyati-Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wace.
17 Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.
18 Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; ndipo anatsika pa buru; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
19 Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwela, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
20 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.
21 Ndipo midzi ya ku malekezero a pfuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwela ndiwo, Kabizeeli ndi Ederi, ndi Yaguri;
22 ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;