2 Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa cigono;
3 nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo mucoke kwanu ndi kulitsata.
4 Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero.
5 Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzacita zodabwiza pakati pa inu.
6 Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la cipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la cipangano, natsogolera anthu.
7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisrayeli onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe.
8 Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la cipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordano muziima m'Yordano.