15 Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali naco coperekedwaco adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo cifukwa analakwira cipangano ca Yehova, ndi cifukwa anacita copusa m'Israyeli.
16 Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israyeli, pfuko ndi pfuko; ndi pfuko la Yuda linagwidwa;
17 nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira cibale ca Azari; nayandikizitsa cibale ca Azari, mmodzi mmodzi, nagwidwa Zabidi;
18 nayandikizitsa a m'nyumba yace mmodzi mmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimu, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda anagwidwa.
19 Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, ucitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israyeli, numlemekeze iye; nundiuze tsopano, wacitanji? usandibisire.
20 Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndacimwira Yehova Mulungu wa Israyeli, ndacita zakuti zakuti;
21 pamene ndinaona pazofunkha maraya abwino a ku Babulo, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi cikute cagolidi, kulemera kwace masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pacepo.