10 ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;
11 ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ace pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babulo.
12 Ndipo pambuyo pace pa kutengedwako ku Babulo, Yekoniya anabala Salatieli; ndi Saiatieli anabala Zerubabele;
13 ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;
14 ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi;
15 ndi Eliyudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;
16 ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wace wa Mariya, amene Yesu, wochedwa Kristu, anabadwa mwa iye.