13 ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;
14 ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi;
15 ndi Eliyudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;
16 ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wace wa Mariya, amene Yesu, wochedwa Kristu, anabadwa mwa iye.
17 Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babulo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babulo kufikira kwa Kristu mibadwo khumi ndi inai.
18 Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.
19 Koma Yosefe, mwamuna wace, anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri,