6 iyeyo sadzalemekeza atate wace. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu.
7 Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndikuti,
8 Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao;Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.
9 Koma andilambira Ine kwacabe,Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
10 Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;
11 si cimene cilowa m'kamwa mwace ciipitsa munthu; koma cimene cituruka m'kamwa mwace, ndico ciipitsa munthu.
12 Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva conenaco?