2 nati, Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda? cifukwa tinaona nyenyezi yace kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.
3 Ndipo Herode mfumuyo pakumva ici anabvutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.
4 Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe akuru onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Kristuyo?
5 Ndipo anamuuza iye, M'Betelehemu wa Yudeya; cifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,
6 Ndipo iwe: Betelehemu, dziko la Yudeya,Sukhala konse wamng'onong'ono mwa akuru a Yudeya.Pakuti Wotsogolera adzacokera mwaiwe,Amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.
7 Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yace idaoneka nyenyeziyo.
8 Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye.