1 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anaturuka mamawa kuka lembera anchito a m'munda wace wampesa.
2 Ndipo parnene adapangana ndi anchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza ku munda wace.
3 Ndipo anaturuka dzuwa litakwera, naona ena ataima cabe pabwalo;
4 ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani cimene ciri coyenera. Ndipo iwo anapita.
5 Ndiponso anaturuka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nacita cimodzimodzi.
6 Ndipo poyandikira madzulo anaturuka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse cabe?
7 Iwo ananena kwa iye, Cifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso ku mundawo wampesa.