11 Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,
12 nati, Omarizira awa anagwira nchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi: kutentha kwace.
13 Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi?
14 Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womarizira monga kwa iwe.
15 Sikuloleka kwa ine kodi kucita cimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi cifukwa ine ndiri wabwino?
16 Comweco omarizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omarizira.
17 Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khurni ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,