30 Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.
31 Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenga kodi comwe cinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,
32 Ine ndiri Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.
33 Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi ciphunzitso cace.
34 Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.
35 Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,
36 Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo?