35 Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,
36 Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo?
37 Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.
38 Ili ndilo lamulo lalikuru ndi loyamba.
39 Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
40 Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo cilamulo conse ndi aneneri.
41 Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa,