18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira zitacitidwa zonse.
19 Cifukwa cace yense wakumasula limodzi la malangizo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu comweco, adzachulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakucita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzachulidwa wamkuru mu Ufumu wa Kumwamba.
20 Pakuti ndinena ndi inu, ngati cilungamo canu sicicuruka coposa ca alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.
21 Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu:
22 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wace wopanda cifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wace, Wopanda pace iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akuru: koma amene adzati, Citsiru iwe: adzakhala wopalamula gehena wamoto.
23 Cifukwa cace ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe,
24 usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nucoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.