3 Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu acitira Mulungu mwano.
4 Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Cifukwa canji mulinkuganizira zoipam'mitimayanu?
5 pakuti capafupi nciti, kunena, Macimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka nuyende?
6 Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa munthu pansi pano za kukhululukira macimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge chika lako, numuke kunyumba kwako.
7 Ndipo ananyamuka, napita ku nyumba kwace.
8 Ndipo m'mene anthu a makamu anaciona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
9 Ndipo Yesu popita, kucokera kumeneko, anaona munthu, dzina lace Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.