12 Koma m'masiku ako sindidzatero cifukwa ca Davide atate wako, koma ndidzaung'ambira m'manja mwa mwana wako;
13 komatu sindidzacotsa ufumu wonsewo; pfuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi cifukwa ca Yerusalemu amene ndinamsankha.
14 Ndipo Yehova anamuutsira Solomo mdani, ndiye Hadadi M-edomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu.
15 Pakuti pamene Davide adali m'Edomu, ndipo Yoabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse m'Edomu;
16 pakuti Yoabu ndi Aisrayeli onse anakhalako miyezi isanu ndi umodzi, mpaka atawapha amuna onse m'Edomu;
17 Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wace pamodzi naye, kumka ku Aigupto, Hadadiyo akali mwana.
18 Ndipo anacoka ku Midyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Aigupto kwa Farao mfumu ya Aigupto, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.