2 Ndipo iye anapfuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lace ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.
3 Ndipo iye anapatsa cizindikilo tsiku lomwelo, nari, Cizindikilo cimene Yehova ananena ndi ici, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa liri pa ilo lidzatayika.
4 Ndipo kunacitika, pa kumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawapfuula, kutemberera guwa la nsembe m'Beteli, Yerobiamu anatansa dzanja lace ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lace analitansira kwa iye linauma, kuti sanatha kulipfunyatitsanso.
5 Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika, monga mwa cizindikilo cimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Mulungu.
6 Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.
7 Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.
8 Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowa kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.