22 koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.
23 Ndipo kunacitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pa buru mneneri amene anambwezayo.
24 Ndipo atacoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha, ndipo mtembo wace unagwera m'njiramo, buru naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.
25 Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m'njiramo, ndi mkango uli ciimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m'mudzi m'mene munakhala mneneri wokalamba uja.
26 Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvera mau a Yehova; cifukwa cace Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.
27 Iye nanena ndi ana ace, nati, Ndimangireni mbereko pa buru. Namangira mbereko.
28 Namuka iye, napeza mtembo wace wogwera m'njira, ndi buru ndi mkango ziti ciimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula buru.