6 Ndipo kunacitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ace alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobiamu, wadzizimbaitsiranji? pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa.
7 Kauze Yerobiamu, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndingakhale ndinakukulitsa pakati pa anthu, ndi kukukhalitsa mfumu ya anthu anga Aisrayeli,
8 ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanana ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wace wonse kucita zolunjika zokha zokha pamaso panga;
9 koma wacimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu yina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;
10 cifukwa cace, taona, ndidzafikitsa coipa pa nyumba ya Yerobiamu, ndi kugurula mwana wamwamuna yense wa Yerobiamu womangika ndi womasuka m'Israyeli, ndipo ndidzacotsa psiti nyumba yonse ya Yerobiamu, monga munthu acotsa ndowe kufikira idatha yonse.
11 Agaru adzadya ali yense wa Yerobiamu wakufa m'mudzi; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova.
12 Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m'mudzi mwanayo adzatsirizika.