16 Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokha zokha m'dzina la Yehova?
17 Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi ziribe mwini, yense abwerere ndi mtendere ku nyumba yace.
18 Pamenepo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Kodi sindinakuuza kuti uyu sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa?
19 Ndipo anati, Cifukwa cace tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wace wacifumu, ndi khamu lonse la Kumwamba liri ciriri m'mbali mwace, ku dzanja lamanja ndi lamanzere,
20 Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Gileadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.
21 Pamenepo mzimu wina unaturuka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Nati Yehova kwa iye, Motani?
22 Nati, Ndidzaturuka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ace onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; turuka, ukatero kumene.