33 Ndipo anthu anu Aisrayeli akawakantha adani ao cifukwa ca kucimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, lodi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;
34 pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira cimo la anthu anu Aisrayeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.
35 Pamene kumwamba kwatsekeka, ndipo kulibe mvula cifukwa ca kucimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;
36 pamenepo mverani Inu m'Mwamba, ndi kukhululukira cimo la akapolo anu, ndi la, anthu anu Aisrayeli; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula pa: dziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale colowa cao.
37 M'dziko mukakhala odala, mukakhala mliri, mlaza, cinoni, dzombe, kapena kapuci, adani ao akawamangira misasa m'dziko la midzi yao, mukakhala mliri uti wonse, kapena nthenda;
38 tsono pempho ndi pembedzero liri lonse akalipempha munthu ali yense, kapena anthu anu onse Aisrayeli, pakuzindikira munthu yense cinthenda ca mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ace ku nyumba yino;
39 pamenepo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kucita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zace zonse, amene Inu mumdziwa mtima wace, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;