25 Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asaturuke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka ku mudzi wa nyumba ya Baala.
26 Naturutsa zoimiritsa zija zinali m'nyumba ya Baala, nazitentha.
27 Nagamula fane la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.
28 Momwemo Yehu anaononga Baala m'Israyeli.
29 Koma Yehu sanazileka zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene adacimwitsa nazo Israyeli, ndizo ana a ng'ombe agolidi okhala m'Beteli ndi m'Dani.
30 Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wacita bwino, pocita coongoka pamaso panga, ndi kucitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli.
31 Koma Yehu sanasamalira kuyenda m'cilamulo ca Yehova Mulungu wa Israyeli ndi mtima wace wonse; sanaleka zoipa za Yerobiamu, zimene anacimwitsa nazo Israyeli.