17 Ndipo Yehoyada anacita cipangano pakati pa Yehova ndi mfomu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.
18 Namuka anthu onse a m'dzikomo ku nyumba ya Baala, naigumula; maguwa ace a nsembe ndi mafano ace anawaswaiswa, napha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova.
19 Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m'dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu ku nyumba ya Yehova, nadzera njira ya cipata ca otumikira, kumka ku nyumba ya mfomu. Nakhala Iye pa cimpando ca mafumu.
20 Nakondwerera anthu onse a m'dziko, ndi m'mudzi munali phe; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.
21 Yoasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.