1 Caka cakhumi ndi ziwiri ca Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.
2 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israyeli asanakhale iye.
3 Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asuri kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.
4 Koma mfumu ya Asuri anampeza Hoseya alikucita ciwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Aigupto, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asuri, monga akacita caka ndi caka; cifukwa cace mfumu ya Asuri anamtsekera, nammanga m'kaidi.