22 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ace, sanayenda m'njira ya Yehova.
23 Ndipo anyamata ace a Amoni anamcitira ciwembu, napha mfumuyo m'nyumba yace yace.
24 Koma anthu a m'dzikomo anapha onse akumcitira ciwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m'dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wace m'malo mwace.
25 Macitidwe ena tsono a Amoni adawacita, salembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
26 Naikidwa iye m'manda mwace m'munda wa Uza; nakhalamfumum'malo mwace Yosiya mwana wace.