14 Musamasautsa wolembedwa nchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu.
15 Pa tsiku lace muzimpatsa kulipira kwace, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wace ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhaireni cimo.
16 Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere cimo lace lace.
17 Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga cikole cobvala ca mkazi wamasiye;
18 koma muzikumbukila kuti munali akapolo m'Aigupto, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; cifukwa cace ndikuuzani kucita cinthu ici.
19 Mutasenga dzinthuzanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'nchito zonse za manja anu.
20 Mutagwedeza mtengo wanu wa azitona musayesenso nthambi mutatha nazo; akhale a mlendo, a mwana wamasiye, ndi a mkazi wamasiye.