9 Amene anati za atate wace ndi amai wace, Sindinamuone;Sanazindikira abale ace,Sanadziwa ana ace omwe;Popeza anasamalira mau anu, Nasunga cipangano canu.
10 Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu,Ndi Israyeli cilamulo canu;Adzaika cofukiza pamaso panu,Ndi nsembe yopsereza yamphumphu pa guwa la nsembe lanu.
11 Dalitsani, Yehova, mphamvu yace,Nimulandire nchito ya manja ace;Akantheni m'cuuno iwo akumuukira,Ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.
12 Za Benjamini anati,Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi iye mokhazikika;Amphimba tsiku lonse,Inde akhalitsa pakati pa mapewa ace.
13 Ndipo za Yosefe anati,Yehova adalitse dziko lace;Ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame,Ndi madzi okhala pansipo;
14 Ndi zipatso zofunikatu za dzuwa,Ndi zomera zofunikatu za mwezi,
15 Ndi zinthu zoposa za mapiri akale,Ndi zinthu zofunikatu za zitunda zosatha,