1 Ndipo ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu anatenga yense mbale yace ya zofukiza, naikamo moto, naikapo cofukiza, nabwera nao pamaso pa Yehova moto wacilendo, umene sanawauza.
2 Ndipo panaturuka moto pamaso pa Yehova, nuwatha, nafa iwo pamaso pa Yehova.
3 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ici ndi cimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala cete.
4 Ndipo Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwacotse pakhomo pa malo opatulika kumka nao kunja kwa cigono.