2 Cilamulo ca wakhate tsiku la kumyeretsa kwace ndi ici: azidza naye kwa wansembe;
3 ndipo wansembe aturuke kumka kunja kwa cigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda Yakhate yapola pa wakhateyo;
4 pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi, ubweya wofiira, ndi hisope;
5 ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;
6 natenge nbalame yamoyo, ndi mtengo wankungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, nazibviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;
7 nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lace, namuche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.
8 Ndipo iye wakutiayeretsedwe atsuke zobvala zace, namete tsitsi lace lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kucigono, koma agone pa bwalo la hema wace masiku asanu ndi awiri.