4 pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi, ubweya wofiira, ndi hisope;
5 ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;
6 natenge nbalame yamoyo, ndi mtengo wankungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, nazibviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;
7 nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lace, namuche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.
8 Ndipo iye wakutiayeretsedwe atsuke zobvala zace, namete tsitsi lace lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kucigono, koma agone pa bwalo la hema wace masiku asanu ndi awiri.
9 Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lace lonse la pamutu pace, ndi ndebvu zace, ndi nsidze zace, inde amete tsitsi lace lonse; natsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nakhale woyera.
10 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge ana a nkhosa awiri, amuna opanda cirema, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamkazi wa caka cimodzi wopanda cirema, ndi atatu a magawo khumi a ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa mafuta.