43 Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m'nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m'nyumba namatanso;
44 pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa.
45 Ndipo apasule nyumbayo, miyala yace, ndi mitengo yace, ndi dothi lace lonse kumudzi kuzitaya ku malo akuda.
46 Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ace iriyotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
47 Ndipo iye wakugona m'nyumbayo atsuke zobvala zace; ndi iye wakudya m'nyumbayo atsuke zobvala zace.
48 Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aiche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.
49 Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;